Psalms 57:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mundichitire chifundo Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti mtima wanga ukudalira Inu. Ndidzathaŵira pansi pa mapiko anu, mpaka chiwonongeko chitandipitirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Altasheti; Mikitamu wa Davide: muja anathawa Saulo, ali m'phanga. Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga. Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo, pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo. Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu mpaka chiwonongeko chitapita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mundicitire cifundo, Mulungu, mundicitire cifundo; Pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu: Ndipo ndithawira ku mthunzi wa mapiko anu, Kufikira zosakazazo zidzapita.