Psalms 57:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo aja adatchera mapazi anga ukonde. Mtima wanga umavutika kwambiri. Akumba mbuna m'njira yanga, koma agweramo okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anatchera mapazi anga ukonde ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa. Anakumba dzenje mʼnjira yanga koma agweramo okha mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anandichera ukonde apo ndiyenda; Moyo wanga wawerama: Anandikumbira mbuna patsogolo panga; Anagwa m'kati mwace iwo okha.