Psalms 59:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
muŵakwiyire ndi kuŵaononga. Muŵaonongeretu kuti asakhaleponso, anthu azidziŵa kuti Mulungu ndiye wolamulira Yakobe, mpaka ku mathero a dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti. Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza m'Yakobo, kufikira malekezero a dziko la pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
muwawononge mu ukali (wanu) muwawononge mpaka atheretu. Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi kuti Mulungu amalamulira Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muwathe mumkwiyo, muwagurule psiti: Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza m'Yakobo, Kufikira malekezero a dziko la pansi.