Psalms 59:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndidzaimba nyimbo zotamanda mphamvu zanu, m'maŵa ndidzaimba mokweza nyimbo zoyamika chikondi chanu chosasinthika. Pakuti Inu mwakhala ngati linga langa ndi malo othaŵiramo pa nthaŵi ya mavuto anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu; inde ndidzaimbitsa chifundo chanu mamawa, pakuti Inu mwakhala msanje wanga, ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ine ndidzayimba za mphamvu yanu, mmawa ndidzayimba zachikondi chanu; pakuti ndinu linga langa, pothawirapo panga mʼnthawi ya mavuto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine, ndidzayimbira mphamvu yanu; Inde ndidzayimbitsa cifundo canu mamawa: Pakuti Inu mwakhala msanje wanga, Ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.