Psalms 59:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu wa Israele. Dzambatukani kuti mulange anthu onse akunja. Musasiye ndi mmodzi yemwe mwa anthu onyengawo, ochita chiwembu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele. Ukani kukazonda amitundu onse, musachitire chifundo mmodzi yense wakuchita zopanda pake monyenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, dzidzutseni nokha kuti mulange anthu a mitundu ina yonse; musaonetse chifundo chanu kwa anthu oyipa achinyengowa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Ukani kukazonda amitundu onse: Musacitire cifundo mmodzi yense wakucita zopanda pace monyenga.