Psalms 60:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Mulungu mwatitaya ife, mwatiwonongera otiteteza. Mwatikwiyira, tibwezeni mwakale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Susan-Eduti. Mikitamu wa Davide; lakulangiza; muja analimbana nao Aramu Naharaimu ndi Aramu Zoba, nabwera Yowabu anapha a Edomu kuchigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu ziwiri. Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; mwakwiya; tibwezereni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere. Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza. Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; Mwakwiya; tibwezereni.