Psalms 60:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mowabu adzakhala ngati mbale yosambiramo ine. Edomu adzakhala poponda nsapato zanga. Ndidzafuula mokondwa nditagonjetsa Filistiya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mowabu ndi mbale yanga yosambira, pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga, pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Moabu ndiye mkhate wanga; Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga: Filistiya, pfuulatu cifukwa ca ine.