Psalms 61:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka; tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ku malekezero a dziko lapansi ndidzapfuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga: Nditsogolereni ku thanthwe londiposa ine m'kutalika kwace.