Psalms 62:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi nonsenu mudzaukira munthu mpaka liti, kuti mumgwetse pansi ngati khoma lopendekeka, ngati mpanda wogwedezeka?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti, kumupha iye, nonsenu, monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti? Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba, ngati mpanda wogwedezeka?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudzambvumbvulukira munthu mpaka liti, Kumupha iye, nonsenu, Monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?