Psalms 62:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Cholinga chao nchongofuna kumtsitsa pa malo ake aulemu. Amakonda kulankhula zonama. Amadalitsa ndi pakamwa pao, koma mumtima mwao amatemberera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo akufunitsitsa kumugwetsa kuti achoke pa malo ake apamwamba. Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza. Ndi pakamwa pawo amadalitsa koma mʼmitima yawo amatemberera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu amkhaliraupo kuti amkankhire pansi ulemu wace; Akondwera nao mabodza; Adalitsa ndi m'kamwa mwao, Koma atemberera mumtima.