Psalms 63:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Salimo la Davide; muja anakhala m'chipululu cha Yuda Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda. Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kuca: Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, M'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.