Psalms 64:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amalimbikira za chiwembu chao, amakambirana zoti atche misampha yobisika, amanena kuti, “Angatiwone ndani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Alimbikitsana m'chinthu choipa; apangana za kutchera misampha mobisika; akuti, Adzaiona ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa, amayankhula zobisa misampha yawo; ndipo amati, “Adzayiona ndani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Alimbikitsana m'cinthu coipa; Apangana za kuchera misampha mobisika; Akuti, Adzaiona ndani?