Psalms 65:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mumathirira kwambiri makwaŵa am'mizere, mumasalaza nthumbira zake, mumafeŵetsa nthaka ndi mvula, ndipo mumadalitsa mbeu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukhutitsa nthaka yake yolima; mufafaniza nthumbira zake; muiolowetsa ndi mvumbi; mudalitsa mmera wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake, mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukhutitsa nthaka yace yolima; Mufafaniza nthumbira zace? Muiolowetsa ndi mbvumbi; Mudalitsa mmera wace.