Psalms 65:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngwodala munthu amene Inu mumamsankha nkubwera naye kudzakhala m'mabwalo anu. Mutikhutitse ndi zinthu zabwino za m'Nyumba yanu, Nyumba yanu yoyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Odala iwo amene inu muwasankha ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu! Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu, za mʼNyumba yanu yoyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, Akhale m'mabwalo anu: Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, Za m'malo oyera a Kacisi wanu.