Psalms 65:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Inu mumatiyankha potipulumutsa ndi ntchito zanu zodabwitsa, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu. Anthu a pa dziko lonse lapansi ndiponso a patsidya pa nyanja zakutali, onsewo amakhulupirira Inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo, Mulungu wa chipulumutso chathu; ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi, ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudzatiyankha nazo zoopsa m'cilungamo, Mulungu wa cipulumutso cathu; Ndinu cikhulupiriko ca malekezero Onse a dziko lapansi, Ndi ca iwo okhala kutali kunyanja: