Psalms 65:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero okhala ku malire akutali a dziko lapansi amaopa zizindikiro zanu zodabwitsa. Anthu amafuula mokondwera chifukwa cha zochita zanu, kuyambira mbali imodzi ya dziko lapansi mpaka mbali yake inanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzachita mantha chifukwa cha zizindikiro zanu; mukondweretsa apo patulukira dzuwa, ndi apo lilowera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu; kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera. Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzacita mantha cifukwa ca zizindikilo zanu; Mukondweretsa apo paturukira dzuwa, ndi apo lilowera.