Psalms 65:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Inu mumadalitsa dziko lapansi ndi kulithirira, ndipo mumalilemeza kwambiri. Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi, Inu mumaŵapatsa anthu dzinthu, pakuti ndimo m'mene mwalikonzera dzikolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeza kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi, muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira; Inuyo mumalilemeretsa kwambiri. Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi kuti upereke tirigu kwa anthu, pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muceza nalo dziko lapansi, muhthirira, Mulilemeza kwambiri; Mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi: Muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.