Psalms 66:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye amalamula ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amalonda mitundu ina ya anthu. Anthu oukira asadzikweze.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Achita ufumu mwa mphamvu yake kosatha; maso ake ayang'anira amitundu; opikisana ndi Iye asadzikuze.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina. Anthu owukira asadzitukumule.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Acita ufumu mwa mphamvu yace kosatha; Maso ace ayang'anira amitundu; Opikisana ndi Iye asadzikuze.