Psalms 68:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe phiri la nsonga zambiriwe, chifukwa chiyani ukuliyang'ana mwansanje phiri limene Mulungu adasankha kuti azikhalapo? Ndithu Chauta adzakhalapo mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri, pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira, kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mucitiranji nsanje mapiri inu a mitu mitu, Ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.