Psalms 68:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzudzulani zilombo zija zokhala m'mabango, ndiponso gulu la nkhunzi lija ndi malikonyani, ndiye kuti akalonga ndi anthu ao. Ponderezani amene amalakalaka ndalama moipa. Abalalitseni anthu okonda nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzudzulani chirombo pakati pa mabango, gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu. Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva. Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dzudzulani cirombo ca m'bango, Khamu la mphongo ndi zipfulula za anthu, Yense wakudzigonjera ndi ndarama zasiliva; Anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.