Psalms 69:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta. Mundiyankhe pa nthaŵi yabwino, Inu Mulungu, chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, ndi chithandizo chanu chokhulupirika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu, mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye, pa nthawi yanu yondikomera mtima; mwa chikondi chanu chachikulu Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine, pemphero langa liri kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa cifundo canu cacikuru, Mundibvomereze ndi coonadi ca cipulumutso canu.