Psalms 69:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mumadziŵa m'mene anthu amandinyozera, m'mene amandichititsira manyazi ndi kundichotsera ulemu. Adani anga onse mumaŵadziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudziwa chotonza changa, ndi manyazi anga, ndi chimpepulo changa. Akundisautsa ali pamaso panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera, kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudziwa cotonza canga, ndi manyazi anga, ndi cimpepulo canga: Akundisautsa ali pamaso panu,