Psalms 69:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtima wanga wasweka chifukwa cha zipongwe, ndataya mtima kotheratu. Ndidafunafuna ena ondichitira chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe. Ndidafunafunanso ena ondisangalatsa, koma sindidampeze ndi mmodzi yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mnyozo waswa mtima wanga ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse; ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cotonza candiswera mtima, ndipo ndidwala ine; Ndipo ndinayembekeza wina wondicitira cifundo, koma palibe; Ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.