Psalms 69:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, ndipo adzamanganso mizinda ya Yuda. Anthu ake adzakhala kumeneko, ndipo lidzakhala dziko lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, nadzamanga midzi ya Yuda; ndipo iwo adzakhala komweko, likhale laolao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni ndi kumanganso mizinda ya Yuda, anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, nadzamanga midzi ya Yuda; Ndipo iwo adzakhala komweko, likhale lao lao.