Psalms 69:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu odana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kupambana tsitsi la kumutu kwanga. Ndi amphamvu anthu ongofuna kundiwononga, ndi kundineneza ndi mabodza ao. Kodi ndiyenera kubweza zimene sindinabe?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amene amadana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga; ambiri ndi adani anga popanda chifukwa, iwo amene akufunafuna kundiwononga. Ndikukakamizidwa kubwezera zomwe sindinabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ondida kopanda cifukwa acuruka koposa tsitsi la pamutu panga; Ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu: Pamenepo andibwezetsa cosafunkha ine.