Psalms 69:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, musalole kuti ndiŵachititse manyazi anthu okhulupirira Inu. Inu Mulungu wa Israele, musalole kuti anthu okufunafunani anyozeke chifukwa cha ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo akuyembekeza Inu, Ambuye Yehova wa makamu, asachite manyazi chifukwa cha ine, iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israele, asapepulidwe chifukwa cha ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amene amadalira Inu asanyozedwe chifukwa cha ine, Inu Ambuye Wamphamvuzonse. Iwo amene amafunafuna Inu asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine, Inu Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo akuyembekeza Inu, Ambuve Yehova wa makamu, asacite manyazi cifukwa ca ine: Iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israyeli, asapepulidwe cifukwa ca ine.