Psalms 7:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wanga, ndikuthaŵira kwa Inu. Mundilanditse kwa onse ondithamangitsa. Mundipulumutse,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Syigayoni wa Davide woimbira Yehova, chifukwa cha mau a Kusi Mbenjamini. Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu; mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sigioni wa Davide, amene anayimbira Yehova zokhudza Kusi, wa fuko la Benjamini. Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu; pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu: Mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;