Psalms 70:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu, azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; nanene kosalekeza iwo akukonda chipulumutso chanu, abuke Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma onse amene akufunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; Nanene kosalekeza iwo akukonda cipulumutso canu, Abuke Mulungu.