Psalms 71:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu; Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga, ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu munandigwirizizakuyambira ndisanabadwe: Kuyambira pa thupi la mai wanga wondicitira zokoma ndinu; Ndidzakulemekezani kosalekeza.