Psalms 72:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'dziko mukhale chakudya chambiri, pamwambanso pa mapiri pakhale dzinthu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni, anthu ake achuluke m'mizindamo ngati udzu wakuthengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse; pamwamba pa mapiri pakhale tirigu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni; zichuluke ngati udzu wakuthengo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzocuruka pamwamba pa mapiri; Zipatso zace zidzati waa, ngati za ku Lebano: Ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.