Psalms 72:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzina lake lisaiŵalike konse, mbiri yake ikhalepobe monga momwe limakhalira dzuŵa. Anthu alandire madalitso chifukwa cha iyo, a mitundu yonse aitche yodala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzina lake likhazikike kwamuyaya, lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa. Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye ndipo iwo adzamutcha iye wodala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dzina lace lidzakhala kosatha: Momwe likhalira dzuwa dzina lace lidzamvekera zidzukulu: Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; Amitundu onse adzamucha wodala.