Psalms 74:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbukirani, Inu Chauta, kuti adani amakunyodolani, kuti anthu achipongwe amanyoza dzina lanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukumbukire ichi, Yehova, mdaniyo anatonza, ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova, momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukumbukile ici, Yehova, mdaniyo anatonza, Ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.