Psalms 74:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zizindikiro zonse za fuko lathu zaonongeka, kulibenso mneneri ndi mmodzi yemwe, palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu amene akudziŵa nthaŵi yodzatha zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sitiziona zizindikiro zathu; palibenso mneneri; ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa; palibe aneneri amene atsala ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sitiziona zizindikilo zathu; Palibenso mneneri; Ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.