Psalms 75:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tikukuthokozani Inu Mulungu, ndithu tikukuthokozani. Tikutchula dzina lanu mopemphera ndipo tikulalika ntchito zanu zodabwitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; Altasyeti; Salimo la Asafu. Nyimbo. Tikuyamikani Inu, Mulungu; tiyamika, pakuti dzina lanu lili pafupi; afotokozera zodabwitsa zanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo. Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tikuyamikani Inu, Mulungu; Tiyamika, pakuti dzina lanu liri pafupi; Afotokozera zodabwiza zanu,