Psalms 75:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'manja mwa Chauta mulitu chikho cha vinyo wofanizira chilango chake, vinyo wotutuma ndi wothirako dzoŵaŵa. Adzatsanyula vinyoyo, ndipo oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa, nadzagugudiza mpaka ndungundungu zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti m'dzanja la Yehova muli cikho; Ndi vinyo wace acita thobvu; Cidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako: Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa Nadzagugudiza nsenga zace.