Psalms 78:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sitidzabisira ana ao, koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo ntchito zotamandika za Chauta, tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa zimene wakhala akuchita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sitidzabisira ana awo, tidzafotokozera mʼbado wotsatira ntchito zotamandika za Yehova, mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sitidzazibisira ana ao, Koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, Ndi mphamvu yace, ndi zodabwiza zace zimene anazicita.