Psalms 78:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adagwetsa moto wa ukali wake pa iwo: adaŵapsera mtima naŵakwiyira nkuŵagwetsera mavuto. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo oononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anawatumizira mkwiyo wake wotentha, kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, ndizo gulu la amithenga ochita zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo, anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anawatumizira mkwiyo wace wotentha, Kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, Ndizo gulu la amithenga ocita zoipa.