Psalms 78:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asakhale ngati makolo ao, anthu oukira ndi osamvera aja, mbadwo wa anthu amene mitima yao inali yosakhazikika, amene moyo wao unali wosakhulupirika kwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kuti asange makolo ao, ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wao, ndi mzimu wao sunakhazikika ndi Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo asadzakhale monga makolo awo, mʼbado wosamvera ndi wowukira, umene mitima yake inali yosamvera Mulungu, umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kuti asange makolo ao, Ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; Mbadwo wosakonza mtima wao, Ndi mzimu wao sunakhazikika ndi Mulungu.