Psalms 79:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani anthu akunja akuti, “Kodi Mulungu wao ali kuti?” Mulole kuti tiwone Inu mukulipsira mitundu ina ya anthu, chifukwa chokhetsa magazi a atumiki anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao? Kubwezera chilango cha mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsa kudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuti, “Ali kuti Mulungu wawo?” Ife tikuona, zidziwike pakati pa anthu a mitundu ina kuti mumabwezera chilango chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa a atumiki anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao? Kubwezera cilango ca mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsa Kudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu,