Psalms 79:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tithandizeni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, kuti dzina lanu likhale ndi ulemerero. Tipulumutseni, ndipo mutikhululukire zochimwa zathu, kuti dzina lanu lilemekezeke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu, chifukwa cha dzina lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tithandizeni Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu chifukwa cha dzina lanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tithandizeni Mulungu wa cipulumutso cathu, Cifukwa ca ulemerero wa dzina lanu; Ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu, Cifukwa ca dzina lanu.