Psalms 80:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imvani, Inu Mbusa wa Israele, Inu amene mumatsogolera anthu a Yosefe ngati gulu la nkhosa. Inu amene mumakhala pa akerubi ngati pa mpando wanu wachifumu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Syosyanimu; lochita mboni; Salimo la Asafu. Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu. Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli, Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa; Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mbusa wa Israyeli, cherani khutu; Inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; Inu wokhala pa akerubi, walitsani.