Psalms 81:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani m'dziko la Ejipito. Yasamani kukamwa, Ine ndidzakudyetsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukuchotsa kudziko la Ejipito; yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto. Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukucotsa ku dziko la Aigupto; Yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.