Psalms 81:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalipereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene zinkatuluka m'dziko la Ejipito. Ndikumva liwu limene sindidalimve ndi kale lonse, lakuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe, pakutuluka iye kudziko la Ejipito. Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto, kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anaciika cikhale mboni kwa Yosefe, Pakuturuka iye ku dziko la Aigupto: Komwe ndinamva cinenedwe cosadziwa ine.