Psalms 84:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000; Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena, Kukhala inewapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, Kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a coipa,