Psalms 84:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale timba amapeza malo okhalapo, nayenso namzeze amamanga chisa chake m'mene amagonekamo ana ake, pafupi ndi maguwa anu, Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mbawanso inapeza nyumba, ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake, pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu, mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo, ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa, kumene amagonekako ana ake pafupi ndi guwa lanu la nsembe, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mbawanso inapeza nyumba, Ndi namzeze cisa cace coikamo ana ace, Pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,