Psalms 85:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimve zimene Chauta adzalankhula, chifukwa adzalankhula za mtendere kwa anthu ake, kwa anthu ake oyera mtima, ngati sabwereranso ku zopusa zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova; pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake, ndi okondedwa ake; koma asabwererenso kuchita zopusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena; Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake, koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzamva colankhula Mulungu Yehova; Pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ace, ndi okondedwa ace; Koma asabwererenso kucita zapusa.