Psalms 87:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amati, “Pakati pa amene amandidziŵa, ndikutchula Rahabu ndi Babiloni. Ponena za dziko la Filistiya, Tiro ndi Etiopiya, anthu amati, ‘Uje adabadwira kumeneko.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine; taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi; uyu anabadwa komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzachula Rahabu ndi Babulo kwa iwo ondidziwa Ine; Taonani, Filistiya ndi Turo pamodzi ndi Kusi; Uyu anabadwa komweko.