Psalms 88:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, Mpulumutsi wanga, ndimalirira Inu usana ndi usiku, kuti mundithandize.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nyimbo, Salimo la ana a Kora. Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Mahalati Leanoti. Chilangizo cha Hemani Mwezara. Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa, ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Salimo la ana a Kora. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a nyimbo yoti: “Pa Matenda ndi pa Mazunzo.” Ndakatulo ya Hemani, wa banja la Ezara. Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa, usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, Mulungu wa cipulumutso canga, Ndinapfuula pamaso panu usana ndi usiku,