Psalms 88:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndili ngati munthu womsiya yekha pakati pa anthu akufa, ngati munthu wophedwa amene wagona m'manda. Ndili ngati anthu amene Inu simuŵakumbukiranso, popeza kuti ndi ochotsedwa m'manja mwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wotayika pakati pa akufa, ngati ophedwa akugona m'manda, amene simuwakumbukiranso; ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa, monga ophedwa amene agona mʼmanda, amene Inu simuwakumbukiranso, amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wotayika pakati pa akufa, Ngati ophedwa akugona m'manda, Amene simuwakumbukilanso; Ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.