Psalms 89:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zakumwamba ndi zanu, dziko lapansi nalonso ndi lanu. Mudapanga dziko lonse ndi zonse zam'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu; munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; Munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwace.